Back to Journals
Nsanamira za mphamvu ya umwini mu Malawi
1 min readNewwave Group

Nsanamira za mphamvu ya umwini mu Malawi

guidemusic-industrymalawichichewa

1. Nsanamira za mphamvu ya umwini mu Malawi

Kumvetsetsa/Kuzindikira nsanamira za mphamvu ya umwini ndikofunikira kwambiri kwa anthu a luso muno mu Malawi.

Mphamvu ya umwini; mwachidule

Mphamvu ya umwini ku Malawi Kuno imapeleka mphamvu ya padera kwa mlengi kapena mwini wa luso pa ntchito yawo ya zolembalemba, kujambula kapena zokhudza mayimbidwe. Izi zikuphatikizanso kapekedwe ka nyimbo, mawu a nyimbo, zotepa ndi ntchito zina zosonyeza luso.

Cholinga ndi Nthawi

Mphamvu ya umwini imagwira ntchito ziwiri; kulimbikitsa chidwi pa ntchito za luso ndi kuteteza cholowa kapena phindu la ndalama kwa anthu a luso. Ku Malawi kuno, mathero a copyright ndi kufikira imfa ya munthu wa luso ndi kuphatikizapo zaka makumi asanu(50); kuwonetsetsa kuti a kubanja la muthu wa lusoyo apindula nayo ntchito yawo.

Ntchito zotetezedwa

Kumalawi kuno mphamvu ya umwini imateteza ntchito zosiyanasiyana, kuphatikizapo

  • Mapekedwe a nyimbo
  • Mawu a nyimbo
  • Zotepa
  • Mabuku
  • Zojambula
  • Umisiri oyendetsera ma kompyuta

Continue reading