
Kuyamba Kwa Gawo lofalitsa nyimbo
1. Kuyamba Kwa Gawo lofalitsa nyimbo
Gawo lofalitsa nyimbo ndilofunikira kwambiri ku ntchito ya oyimba muno mu Malawi, chifukwa imakhudza mulingo wa anthu amene angafikilidwe ndi phindu la ndalama limene lingapezeke. Mu mayiko olemera ndi amene ali ndi kuchuluka kwa mitundu ya nyimbo pa chikhalidwe chawo, kafalitsidwe koyenera kamawonetsetsa kuti anthu a luso akulumikizana ndi anthu ndikuwathandizira kupeza phindu lowasamala pa moyo wawo.
Kufunika Kofalitsa
Kwa oyimba a chi Malawi, kufalitsa kumatanthauza kuti nyimbo zao zimakawafikira anthu osangalatsidwa mdziko muno komanso kunja kwa dziko lathu. Anthu amakhoza kugawana ndi anthu ena luso limene ali nalo, amatha kufotokozera chikhalidwe, komanso kupeza la mchere. Kupanda ndondomeko zofalitsira moyenerera, anthu a luso akhoza kuzimira ndikusadziwika.
Kufalitsa kwa makolo ndi Kufalitsa kwa Dijito
Mu zaka za mu mbuyomo, kufalitsa nyimbo ku Malawi kuno kumadzera mu ma C.D ndi ma kaseti amene amagulitsidwa ndi ofalitsa ngati OG Issa ndi muma bwalo a msangalutso ndi zisudzo. Masiku ano kufalitsa kupyolera mu njira za dijito ndikumene kwatenga malo,. ndi chithandizo cha malo a pa intaneti ngati Newwave Malawi, amene akulimbikitsa mafalitsidwe a dijito. Kufalitsa mu njira za dijito ndi kwa phindu chikukwa anthu owafikila amakhala ochuluka, kumakhala kotsika mtengo komanso kudziwika ku mayiko ena a mdziko la pansi komakhala kosavuta.