
Kunyozera/kuswa lamulo la mphamvu ya umwini komanso kagwiritsidwe ntchito
3. Kunyozera/kuswa lamulo la mphamvu ya umwini komanso kagwiritsidwe ntchito
Kuteteza mphamvu ya umwini muno mu Malawi kumaphatikizapo kuzindikira ndi kuchitapo kanthu pamene lamulo la mphamvu ya umwini laswedwa.
Kuzindikira kuswedwa kwa mphamvu ya umwini
Alengi akuyenera kukhala ochilimika Poyang’ana momwe nyimbo zawo zikugwiritsidwa ntchito, kuti athe kudziwa ngati mphamvu yawo ya umwini ili pa chiwopysezo. Izi zingathe kuphatikizapo kulimbikitsa momwe zopeka zawo zikuyendera mu malo ogulitsira, kufalitsa kosavomerezeka, kapena kutenga mu matsamba a intaneti kosavomerezeka.
Malalmulo athu amalola kuti ntchito zina zimene zinalembetsedwa mu kaundula wa mphamvu ya umwini zigwiritsidwe ntchito munthu asanapeze chilorezo kuchokera kwa mwini wake wa luso/ntchito, kapena kupereka dipo kwa mwini wake wa ntchito, kwa amane akufuna kuphunzitsira, kuwulutsa nkhani, ndikupanganso ntchito ndicholinga choti anthu amane ali ndi ulumali athe kuyamikira nawo ntchitoyo.
Chithandizo cha Lamulo
Lamulo la mphamvu ya umwini likaswedwa, anthu a luso akhoza ku gwiritsa ntchito nthambi/ ndondomeko ya za malamulo a mu dziko la Malawi. Chithandizo kudzera mu malamulo chimatha kupezeka mu njira yomulipilitsa dipo amene walakwa, kuletsa kupitilira kwa ntchito imene ikutsutsana ndi mphamvu ya umwini kapena kutsata njira zothana ndi mchitidwe wa upandu ngati nkhani ili yonyanyira.
Mbali ya COSOMA
COSOMA imatenga mbali yofunikira pakugwiritsa ntchito lamulo la mphamvu ya umwini mu Malawi. A COSOMA amathandizira kuteteza ufulu wa alengi/ anthu a luso ndikuwasonyeza njira zoyenerera kutsata pofuna kuwasumira anthu amene sanatsate lamulo la mphamvu ya umwini.
Kuphunzitsa ndi Kuzindikiritsa
Pofuna kuti tithane ndi mchitidwe onyozera malamulo a mphamvu ya umwini, COSOMA ndi ma bungwe ena ayenera kugwira ntchito yophunzitsa anthu aluso mphamvu imene ali nayo ndikufunikira kogwiritsa ntchito malamulo a mphamvu ya umwini.