Back to Journals
Kulembetsa mphamvu ya umwini
2 min readNewwave Group

Kulembetsa mphamvu ya umwini

guidemusic-industrymalawichichewa

2. Kulembetsa mphamvu ya umwini

Kulembetsa mphamvu yanu ya umwini ku Malawi kuno si kokakamiza, koma kumapindulitsa.

Ndondomeko yakalembetsedwe

Anthu a lusowa, akuyenera kulembetsa popeleka ziphaso zololedwa ndi bungwe loyang'anila umwini mdziko muno (COSOMA) komanso akuyenera kulipira, po pereka zikalata zoyenerera komanso dipo. Kulembetsa umwini sikokakamiza kuti mphamvu ya umwini ikhale yotetezeka, koma kumathandizila kusonyeza umboni wovomerezeka ndi malamulo a dziko la Malawi. Ku Malawi kuno oyimba amene akufuna kuteteza mphamvu yawo ya umwini ayenera ku lembetsa polemba mu zikalata zokhudzana ndi umwini ku bungwe la Copyright association of Malawi COSOMA:

  • Chikalata choyenereza kulowa mu mbugwe la COSOMA ngati membala

Chikalata ichi chimagwiritsidwa ntchito pofuna kuwonetsa chidwi chofuna kutengapo mbali mu bungwe la COSOMA, ngati membala. Kukhala membala ndikofunikila ngati munthu akufuna kulembetsa mphamvu ya umwini pa ntchito zake za luso.

  • Chikalata cha omwe anagpindule ndi COSOMA

Chimagwiritsidwa ntchito popatulila anthu amene angapindule ndi ndalama zimene zimabwera kudzera mu ntchito zimene zinalembetsedwa mu kaundula wa mphamvu ya umwini

  • Chikalata chowonetsera ntchito

Chimagwiritsidwa ntchito pofuna kufotokozera ntchito zimene munthu wa luso akufuna kuteteza polembetsa mu kaundula wa mphamvu ya umwini. Wolembetsa ayenera kufotokozera ntchito iliyonse kuyambira mutu kapena dzina la ntchito, dzina la wolenga ndi kenakalikonse kofunikira, kokhudza ntchito zo.

Continue reading