Back to Journals
Kufalitsa mwa dijito(intaneti) muno mu Malawi
3 min readNewwave Group

Kufalitsa mwa dijito(intaneti) muno mu Malawi

guidemusic-industrymalawichichewa

2. Kufalitsa mwa dijito(intaneti) muno mu Malawi

Oyimba a chi Malawi akhoza kutengerapo mwayi ogwiritsa ntchito njira za dijito kuti afikile anthu ambiri mdziko lathu lino komanso ku mayiko ena a kunja kwa dziko lathuli.

Malo ofalitsila nyimbo:

  • Spotify
  • Apple Music
  • BoomPlay
  • YouTube

GKufikitsa nyimbo pa malowa

Anthu a luso loyimba atha kupereka nyimbo zawo ku malowa kudzera mu alumikizi kapena kulumikiza okha ngati iwo akuwona kuti ndondo meko za malo ofalitsirawo azilondoloza bwino lomwe. Alumikizi ngati DistroKid, CDBaby ndi TuneCore atha kuwathandiza anthu a luso kufalitsa nyimbo zawo kuti zifike malo osiyanasiyana. Kuti Nyimbo ziyikidwe ndikufalitsidwa kudzera mu malo olumikiza a dijito, pakuyenera kuchitika zotsatira izi:

  • Kamvekedwe kopambana

Wonetsetsani kuti muli ndi katundu wa nyimbo zanu ndi womveka mwa tyatyatya kuti makina a dijito athe kuyimba nyimbozo mosavutikira. Alumikizi ambiri amafuna kugwiritsa ntchito ma fayilo a WAV or FLAC koma amatha kuwasintha kuti akhale mafayilo oyenerera pofalitsa nyimbo (mwachitsanzo, MP3).

  • Chithunzi chabwino cha pa Chikutilo

Ntchito imene ikufalitsidwa ikuyenera kukutidwa. Chikutilo chake chikhale cha mawonekedwe opambana ochititsa kaso(kawili kawili zithunzi izi zimakhala zokwana mulingo wa ma pikiselo 3000mulitali ndi 3000mofupika) mu kalinganizidwe JPEG kapena PNG. Chithunzi cha pa chikutiro ndi chyambilira chimene anthu amawona akakumaniza ndi nyimbo pa malo omvetsera nyimbo.

  • Kufotokozera nyimbo zanu: imodzi imodzi

Prepare metadata for each track, including:

  1. Dzina la nyimbo
  2. Dzina la munthu wa lusoyo
  3. Dzina la chimbale (ngati chilipo)
  4. Tsiku limene nyimbo inatuluka
  5. Chamba cha nyimbo
  6. Mawu a mu nyimbo(mukhoza kusankha kuyika kapena kusayika)
  7. Ndondomeko zojambulira (ISRC (International Standard Recording Code)), ngati zilipo
  8. Wopeka, wolemba, ndi wosindikiza ndi kugulitsa
  • Nkhani yobvumbulutsa

Ganizirani tsiku lomwe komanso njira zotulutsira monga ndondomeko zoguliratu kapena kusungitsa ntchito isanatulitsidwe. Alumikizi ena amapelaka mpata wopeza nthawi yapadera yotulutsira ntchito/nyimbo.

  • Nkhani ya akaunti

Mukuyenera kukonza akauntindi alumikizi a dijito(pa intaneti) ngati simunatero kale. Izi zikukhudza kufotokozera zambiri yanu panokha komanso njira yomwe mudzitsata polipira. Alumikizi ena amapereka ma mpata wosankha kukhala ndi akaunti ya ulere koma kumagawana nawo phindu limene lingapezeke kupyolera mu akaunti ‘yo.

  • Ndondomeko yolipilira

Mukuyenera kupereka akaunti yanu yaku banki kapena akaunti yanu ya pa intaneti ya PayPal kuti muzipeza malipiro a padera kuchokera kwa amene akugula ndi kumvetsera nyimbo zanu.

  • Nkhani ya msonkho

Ngati nyimbo zikufalitsidwa ku mayiko a kunja, mwina mutha kufunsidwa kuti mupereke ndondomeko ya momwe mumalipilira msonkho monga chizindikiro chanu cha msonkho kapena chikalata (fomu) cha W-8BEN (kwa amene samakhala mu dziko la United States), kuti muyendetse ntchito molingana ndi malamulo a msonkho a kumayiko amene nyimbo zanu zikufalitsidwa.

  • Dipo kwa Alumikizi

Mukhale okonzeka kupereka dipo la ndalama chifukwa chogwiritsa ntchito alumiki. Dipo limeneli litha kuperekedwa ntchito isanagwiridwe, pa chaka kapena kudula muyeso wa peresenti pa phindu la ndalama limene lapezeka.

  • Zikalata za malamulo

Alumikizi ena amafuna kuti kukhazikitsa mgwirizano pakati pa iwo ndi inu wokhudza ndondomeko za kagwiridwe ka ntchito zawo zofalitsa, asanayambe kugwira ntchitoyo. Wonetsetani kuti zikalatazi zawerengedwa bwino lomwe musanasindikize chizindikiro cha kuvomereza kwanu.

  • Chizindikiro chanu cha pa YouTube

Ngati mukukonza ndondomeka yofalitsira nyimbo kudzera pa YouTube, muyenera kufotokoza momwe mukufunira kuti nyimbo zanu zulembetsedwe mukawundula wa zizindikiro za eni luso.

  • Ndondomeko zogawanirana phindu

Kawirikawiri, malo a dijito(intaneti) amatsata ndondomeko zogawanirana phindu la ndalama pomwe anthu a luso amatenga gawo la ndalama zimene zapezeka kupyolera mu kumvetsera kapena kuchotsa (dawunilodi) kwa nyimbo kumene kumachitika. Ndalama izi, zimaperekedwa pa mwezi kapena pa kotala ya miyezi, zimene zimathandiza kuti oyimba apeze phindu mu nyimbo zawo.

Continue reading