Back to Journals
Kufalitsa ndi njira zowoneka ndi maso  muno mu Malawi
2 min readNewwave Group

Kufalitsa ndi njira zowoneka ndi maso muno mu Malawi

guidemusic-industrymalawichichewa

3. Kufalitsa ndi njira zowoneka ndi maso muno mu Malawi

Pamene njira zofalistira za dijito za tenga malo, kufalitsa nyimbo kowoneka ndi maso kudakali kofunikira mu ntchito za oyimba kuno ku Malawi.

Mbali ya mafalitsidwe owoneka ndi maso

Njira za malitsidwe owoneka ndi maso monga kugulitsa ma CD komanso kuyimba pa mawayilesi, kudakali kofunikira kwa anthu a luso amene amakasonyeza ntchito zawo ku mabwalo a msangulutso, ku ziwonetsero za makolo komanso mumisika.

Njira komanso Ndondomeko zofalitsira

Oyimba kuno ku Malawi, akhoza kugwira ntchito ndi sitolo zofalitsa zimene zimatchedwa “Soft Copy Distributors”, zimene zimapezeka ku malo ogulitsira akuluakulu mu dziko muno, mumisika ndi sitolokuti athe kufalitsa nyimbo munjira zowoneka ndi maso. Kukhazikitsa mgwirizano ndi malo oterewa ndi kothandiza koposa. Kuwonjezera apo, kugwirizana ndi anthu olinganiza zochitikachitika kuti azigulitsa ma CD ku malo a zochitikachitika kutha kuchita malonda oposa.

Gawo 29 la lamulo la mphamvu ya umwini, Copyright act limapatula mphamvu mwapadera zoloreza kuchita zotsatira izi:

  • kujambulanso nyimbo zitajambulidwa kale.
  • Kutanthauzira kapena kupereka chithunzithunzi china.
  • Kufalitsa nyimbo zanu.
  • Kuyimba nyimbo zanu ku gulu.
  • Kusonyeza nyimbo zanu ku gulu.
  • Kulankhula ku gulu za nyimbo zanu.

Ndi chifukwa chake kunakhazikitsidwa msonkho umene umayikidwa pa katundu okopela nyimbo monga ma tepi, CD,DVD, Flashi, ma foni a mu manja makina a kompyuta ndi zina, kuti athe kuteteza anthu a luso ku mchitidwe wokopela ntchito ya anthu a luso mosavomerezeka komanso kuti anthu a luso athe kupindula.

Continue reading