
Nsanamira za kusindikiza ndi kugukitsa nyimbo
1. Nsanamira za kusindikiza ndi kugukitsa nyimbo
Kusindikiza ndi kugulitsa nyimbo ndi mbali yofunikira kwambiri mu ntchito za oyimba, imene ikufunika kutukulidwa muno mu Malawi. Kumakhudza kasamalidwe komanso kagulitsidwe ka zopeka mu nyimbo.
Kufunika kosindikiza ndi kugulitsa nyimbo
Kusindikiza ndi kugulitsa nyimbo ndikofunikira kwambiri kwa olemba mawu a mu nyimbo , chifukwa amalandira malipiro nyimbozo zikamagwiritsidwa ntchito. Ndala izi zimathandiza kusamala ntchito yawo komanso luso lawo kwa nthawi yayitali.
Mbali imene osindikiza ndi kugulitsa nyimbo amatenga
Osindikiza ndi kugulitsa nyimbo amakhala ngati mkhala pakati wa olemba nyimbo ndi amene amagwiritsa ntchito nyimbo zawo monga owulutsa mawu kudzera pa wayilesi, ojambula zinthunzi zoyenda ndi otsatsa malonda. Amakanenerera pazokambirana zopereka chilolezo, amatolera malipiro a padera ochokera kwa amene akugwiritsa ntchito nyimbo komanso amawonetsetsa kuti ufulu wa anthu opeka nyimbo sukunyozeka.