Back to Journals
Malipiro ndi Njira Zobweretsera Ndalama
1 min readNewwave Group

Malipiro ndi Njira Zobweretsera Ndalama

guidemusic-industrymalawichichewa

3. Malipiro ndi Njira Zobweretsera Ndalama

Oyimba a mu Malawi muno atha kupeza phindu la ndalama za padera pa ntchito yawo iliyonse mu njira zosiyanasiyana, kuphatikizapo ndalama za padera zochokera ku COSOMA pamene oyimba achita zionetsero za ntchito yawo kapena kuyimba kumagulu kapena khwimbi la anthu, kapena pa wayilesi kapenanso ziwonetsero za pa wayilesi ya kanema kapena ku pa bwalo la gulu la anthu. Akhozanso kulandila ndalama za padera zochokera kwa anthu amene amagulitsa zimbale zogwirika ndi manja kapena za dijito zochokera pa intaneti pojambula mobwerekera kapena kukopera ntchito ya oyimba ena.

Ndalama Za Padera Kuchokera Kunja Kwa Malawi

A Malawi a luso akhoza kupindula popeza ndalama zapadera zochokera ku maiko ena kupyolera mu migwirizano yobwezerana ya pakati pa COSOMA ndi mabungwe a maiko a kunja oyang’anira mphamvu ya umwini. Izi zimawathandizira kupeza ndalama za padera pamene anthu amvetsera kapena kugwiritsa ntchito ntchito zawo mu maiko a kunja.

Continue reading